nya-x-nyanja_1ki_text_reg/14/11.txt

1 line
536 B
Plaintext
Raw Permalink Blame History

This file contains ambiguous Unicode characters

This file contains Unicode characters that might be confused with other characters. If you think that this is intentional, you can safely ignore this warning. Use the Escape button to reveal them.

\v 11 Aliyense wa Yerobiamu amene adzafera mumzindawo, agalu adzamudya, ndipo aliyense wofera kutchire adzamudya ndi mbalame za mmlengalenga, pakuti ine Yehova ndanena zimenezi. \v 12 Chotero nyamuka, mkazi wa Yerobiamu, bwerera kunyumba kwako; mapazi ako akalowa mmudzi, mwana Abiya adzafa. \v 13 Aisiraeli onse adzamulira ndi kumuika mmanda. Ndi iye yekha wa mbanja la Yerobiamu amene adzalowa mmanda, chifukwa mwa iye yekha, mnyumba ya Yerobiamu, munapezeka chilichonse chokoma pamaso pa Yehova Mulungu wa Isiraeli.