\v 11 Aliyense wa Yerobiamu amene adzafera mumzindawo, agalu adzamudya, ndipo aliyense wofera kutchire adzamudya ndi mbalame za m’mlengalenga, pakuti ine Yehova ndanena zimenezi. \v 12 Chotero nyamuka, mkazi wa Yerobiamu, bwerera kunyumba kwako; mapazi ako akalowa m’mudzi, mwana Abiya adzafa. \v 13 Aisiraeli onse adzamulira ndi kumuika m’manda. Ndi iye yekha wa m’banja la Yerobiamu amene adzalowa m’manda, chifukwa mwa iye yekha, m’nyumba ya Yerobiamu, munapezeka chilichonse chokoma pamaso pa Yehova Mulungu wa Isiraeli.