\c 1 \v 1 Icho camene cenzeko kufumila pachiyambi, camene tinamvwa, camene tinaona na menso yatu, chamene tinapenyesesa, camene tinagwila ndi manja yathu - ichi ndiye ca Mau ya moyo. \v 2 Moyo, unazibisidwa, ndipo tauona, ndipo tiucitila umboni. Tikulalikilani kwa inu za umoyo wosatha, wamene unali ndi Atate, ndipo waziwika kwa ife.