\c 2 \v 1 Mwaici ikani pambali vonse viipa, zonse zonyenga, maonekelo onyenga, kukhubwila, na manyozo onse. \v 2 Ngati bana bakhanda, funani mukaka woyela wamuzimu, kuti mwaici mungakule mucipulumuso, \v 3 ngati mwalaba kuti Ambuye nabwino.