\v 2 Ndikanakutsogolera ndi kukulowetsa m'nyumba ya mayi anga, amene anali kundiphunzitsa. Ndikadakumwetsa vinyo wokometsera ndi zakumwa za makangaza anga. Mayiyo akuyankhula yekha \v 3 Dzanja lake lamanzere lili kumutu kwanga ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira.