\v 8 Pali phokoso pali okondewa wanga! Mvelani, apa abwela, akudumpha pamapiri, nakujumpha pamapiri. \v 9 Wokondewa wanga ali ngati mbawala kapena mwana wa mphoyo; onani, wayimirira kuseli kwa khoma lathu, akuyang'anisisa pazenera, asuzumila pazenela.