nya-x-nyanja_rev_text_reg/16/04.txt

1 line
441 B
Plaintext

\v 4 Mngelo wa chitatu anathira mbale yake m'misinje na nyenje za manzi ndipo zinasanduka magazi. \v 5 Ninamvera mgelo wa manzi kukamba ati, "ndinu oyera-amene aliko ndipo analiko, Oyera- chifukwa mwaweruza zinthu izi. \v 6 Chifukwa anathira magazi ya okhulupilira na aneneri, mwabapasa magazi kuti bamwe; ni zamene bayenera. \v 7 Ninamvera guwa kukamba ati, "Inde, ambuye Mulungu a mphamvu zonse, chiweruzo chanu ni ca zoona na cholungama."