\c 5 \v 1 Ndipo ninaona mumanja mwa iye amene anakhala pa mpando wa chimfumu ku dzanja la manja lake, chi buku cholembewa mbali zonse ziwiri. Inali yosindikiziwa na zosindikizira 7. \v 2 Ninaona mngelo wa mphamvu kukuwa ni mau okweza, "Ndani oyenera kusegula buku na zosindikizira zake?"