\c 9 \v 1 Ndipo mngelo wa cisanu analiza lipenga yake. Ninaona nyenyezi kumwamba yamene inagwa pa dziko la pansi. Nyenyezi inapasiwa makiyi yosegulira mugodi opanda kolekezera. \v 2 Inasegula khomo la mugodi opanda kolekezera, ndipo panachoka utsi monga uchoka pa muliro waukulu. Dzuwa na mphepo zinadesedwa chifukwa cha utsi ochokera ku mugodi wamene uyu.