\v 9 Anaimba nyimbo ya sopano: Ndinu oyenera kutenga buku ndi kulisegula zosindikizira zake. Chifukwa munaphedwa, ndipo na magazi anu munagula anthu a mitundu yonse kwa atate, chilankhulo, mtundu, anthu na maiko. \v 10 Munawapanga ufumu, ndi ansembe kutumikira Mulungu wathu, ndipo azakhala pa dziko la pansi."