\v 17 Mukamba kuti, ndinu olemera, nili na zinthu zambiri, ndipo sinifuna kalikonse. Koma simuziba kuti ndinu ochitisa chifundo maningi, osauka, osapenya ni osabvala. \v 18 Mvelani zamene nikamba: Gulani kwa ine golide oikidwa mu moto kuti munkhale olemera na zobvala zoyera zowala kuti mubvale musaonese manyazi ya umaliseche wanu, na mankhwala ya m'maso kuti uone bwino.