\v 3 Kumbukirani, sopano, zamene munalandira na kumvera. Gonjerani, na kulapa. Koma ngati simuzauka, nizabwera monga kawalala, elo simuzaziba nthawi yamene nizabwelera kwa inu. \v 4 Koma pali maina yang'ono chabe ya banthu mu Sardis bamene sibanafipise vovala vao. Bazayenda naine, mu zobvala zoyera, chifukwa nioyenera.