nya-x-nyanja_deu_text_reg/02/30.txt

1 line
366 B
Plaintext

\v 30 Koma Sihoni, mfumu ya Heshboni, sanafune kuleka ife kupitila kuli eve; chifukwa Yehova Mulungu wanu anayumisa maganizo yake na kulimbisa mutima wake, kuti iye angamugonjese mwa mpavu zanu, monga mwamene akuchita lelo. \v 31 Yehova anakamba kuli ine, 'Ona, Ine nayamba kupulumusa Sihoni na malo yake basogolo panu; yambani kutenga, kuti imwe mutenge malo yake.'