nya-x-nyanja_2ch_text_reg/32/24.txt

1 line
509 B
Plaintext

\v 24 Masiku amenewo Hezekiya anadwala mpaka kutsala pang'ono kufa. Iye anapemphera kwa Yehova, amene analankhula naye ndi kumupatsa chizindikiro chakuti iye achira. \v 25 Koma Hezekiya sanabwezere Yehova chifukwa cha thandizo lomwe anam'patsa, pakuti mtima wake unakwezedwa. Pamenepo mkwiyo unamugwera, ndi Yuda ndi Yerusalemu. \v 26 Komabe, Hezekiya pambuyo pake anadzichepetsa chifukwa cha kunyada kwa mtima wake, iye ndi anthu a mu Yerusalemu, kotero kuti mkwiyo wa Yehova sunawagwere m'masiku a Hezekiya.