nya-x-nyanja_2ch_text_reg/32/13.txt

1 line
731 B
Plaintext

\v 13 Kodi simudziwa chimene ine ndi makolo anga tawachitira anthu onse a m'maiko ena? Kodi milungu ya anthu akumayiko oyandikana nayo idakwanitsa kupulumutsa dziko lawo m'manja mwanga? \v 14 Mwa milungu yonse ya mitundu iyi makolo anga anaiwonongeratu, kodi panali mulungu aliyense amene akanakhoza kupulumutsa anthu ake m'manja mwanga? Chifukwa chiyani Mulungu wanu angathe kukupulumutsani mmanja mwanga? \v 15 Tsopano musalole kuti Hezekiya akupusitseni kapena kukunyengererani mwanjira imeneyi. Musamamukhulupirire, chifukwa palibe mulungu wa mtundu uliwonse kapena ufumu uliwonse umene wapulumutsa anthu ake m mymanja mwanga, kapena m ofmanja mwa makolo anga. Koposa kotani nanga Mulungu wanu adzapulumutsa inu m'manja mwanga?