nya-x-nyanja_2ch_text_reg/31/11.txt

1 line
521 B
Plaintext

\v 11 Pamenepo Hezekiya analamula kuti zikonzedwe m'nyumba ya Yehova; ndipo anazikonzeratu. \v 12 Kenako anabweretsa mokhulupirika nsembe zopereka, chakhumi, ndi zinthu za Yehova. Kananiya Mlevi ndiye anali kuwayang'anira, ndipo m'bale wake Simeyi anali wachiwiri wake. \v 13 Yehieli, Azaziya, Nahati, Asaheli, Yerimoti, Yozabadi, Elieli, Isimakiya, Mahati, ndi Benaya anali oyang'anira pansi pa ulamuliro wa Konaniya ndi Simeyi m'bale wake, mwa kuikidwa ndi Hezekiya, mfumu, ndi Azariya, woyang'anira nyumba ya Mulungu .