nya-x-nyanja_2ch_text_reg/31/01.txt

1 line
364 B
Plaintext

\c 31 \v 1 Zonsezi zitatha, anthu onse a mu Israeli amene anali kumeneko anatuluka kupita ku mizinda ya ku Yuda nathyola zipilala zamiyala ndi kudula zipilala za Asera, naphwanya malo okwezeka ndi maguwa ansembe Yuda ndi Benjamini, ndi Efraimu ndi Manase, kufikira atawatha onse. Pamenepo anthu onse a Isiraeli anabwerera, aliyense kumalo ake ndi kumzinda wakwawo.