nya-x-nyanja_2ch_text_reg/32/27.txt

1 line
514 B
Plaintext

\v 27 Hezekiya anali ndi chuma chambiri ndi ulemu waukulu. Anadzipezera zipinda zosungiramo siliva, golide, miyala yamtengo wapatali, ndi zonunkhiritsa, komanso zishango ndi zinthu zosiyanasiyana zamtengo wapatali. \v 28 Anali ndi nkhokwe zosungira tirigu, vinyo watsopano, ndi mafuta, komanso malo osungira ziweto zamitundumitundu. Analinso ndi ziweto m'khola lawo. \v 29 Kuwonjezera apo, anadzipezera mizinda ndi katundu wambiri wa nkhosa ndi ng'ombe, chifukwa Mulungu anali atamupatsa chuma chochuluka kwambiri.