nya-x-nyanja_2ch_text_reg/32/16.txt

1 line
394 B
Plaintext

\v 16 Atumiki a Sanakeribu analankhulanso zinthu zoipa motsutsana ndi Yehova Mulungu ndiponso motsutsana ndi Hezekiya mtumiki wake. \v 17 Senakeribu nayenso analemba makalata pofuna kunyoza Yehova, Mulungu wa Israeli, komanso kumunenera zoipa. Adati, "Monga milungu yamitundu ya m'maiko sinalandire anthu awo m'manja mwanga, momwemonso Mulungu wa Hezekiya sapulumutsa anthu ake m'manja mwanga."