nya-x-nyanja_2ch_text_reg/32/06.txt

1 line
562 B
Plaintext

\v 6 Anaika oyang'anira ankhondo pa anthu. Anawasonkhanitsira kwa iye pabwalo lalikulu pachipata cha mzinda ndipo analankhula nawo molimbikitsa. Iye anati: \v 7 “Limbani mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu. Musaope kapena kutaya mtima chifukwa cha mfumu ya Asuri ndi gulu lonse lankhondo limene ili nalo, chifukwa pali wina amene ali ndi ife woposa amene ali naye. \v 8 Iye ali ndi dzanja la nyama, koma ife tiri ndi Yehova Mulungu wathu, kuti atithandize ndi kutimenyera nkhondo zathu. ”Pamenepo anthuwo analimbikitsidwa ndi mawu a Hezekiya mfumu ya Yuda.