nya-x-nyanja_2ch_text_reg/24/17.txt

1 line
422 B
Plaintext

\v 17 Pambuyo pa imfa ya Yehoyada, asogoleli ba kwa Yuda banabwela na kulemekeza mfumu. Mwaicho mfumu inabanvela. \v 18 Banasiya nyumba ya Yehova, Mulungu wa makolo yabo, na kumpembeza milungu yopatulika na mafano. Ukali wa Mulungu unagwela Yuda na Yerusalemu chifukwa cha kulakwa kwabo. \v 19 Koma anatumiza baneneli kuli beve kuti ababwezelese kuli eve, Yehova; baneneli anachitila umboni antu, koma banakana ku kumvela.