nya-x-nyanja_2ch_text_reg/23/12.txt

1 line
459 B
Plaintext

\v 12 Ataliya ananvela chongo cha bantu kutamanga na kutamanda mfumu, anabwela kuli bantu mu nyumba ya Yehova., \v 13 ndipo anaona, mfumu inaimilila pambali pa chipilala chake pakomo, na bakazembe na kuimba malipenga yanali pafupi na mfumu. Bantu bonse mziko banali kusangalala ndipo banali kuimba malipenga, ndipo oyimba anali kuimba zida zoimbila na kusogolela kuimba nyimbo zotamanda Mulungu. Ataliya anangamba vovala vake na kupunda, "Chiwembu! Chiwembu!"