nya-x-nyanja_2ch_text_reg/14/12.txt

1 line
323 B
Plaintext

\v 12 Momwemo Yehova anakantha Akusi pamaso pa Asa ndi Yuda; Akusi anathawa. \v 13 Asa ndi asilikali amene anali naye anawathamangitsa mpaka ku Gerari. Chotero akusi ambiri anaphedwa moti sanathenso kuchira, pakuti anawonongedwa kotheratu pamaso pa Yehova ndi gulu lake lankhondo. Gulu lankhondo linatenga zofunkha zambiri.