nya-x-nyanja_2ch_text_reg/13/13.txt

1 line
398 B
Plaintext

\v 13 Koma Yerobiamu anakonzera olalira pambuyo pao; ankhondo ake anali patsogolo pa Yuda, ndipo obisalirawo anali pambuyo pawo. \v 14 Pamene Yuda anacheuka, taonani, nkhondo inali patsogolo pao ndi pambuyo. Iwo anafuulira Yehova, ndipo ansembe analiza malipenga. \v 15 Pamenepo amuna a Yuda anapfuula; pamene anali kufuulira, Yehova anakantha Yerobiamu ndi Aisrayeli onse pamaso pa Abiya ndi Yuda.