nya-x-nyanja_1ki_text_reg/08/46.txt

1 line
496 B
Plaintext

\v 46 Tiyelekeze kuti bakukuchimwilani, popeza palibe wamene samachimwa, ndipo muganiza kuti mwabakwiyila nakubapeleka mumanja mwa badani, kotelo kuti mudani wamene uyo azabatenga ukapolo kuziko yawo, ngakhale kutali kapena pafupi. \v 47 Ndiye ganizilani kuti bakumbukila kuti bali muziko yamene banatengewa ukapolo, nakuganiza kuti balapila nakupempha chifundo kwa imwe kuchokela kuziko ya bamene banabatenga. Tiyelekeze kuti banakamba, 'Tachita zolakwa ndipo tachimwa. Tachita vinthu voipa. '