nya-x-nyanja_1ki_text_reg/08/29.txt

1 line
404 B
Plaintext

\v 29 Maso anu akhale otsegukira kukachisi uyu usiku ndi usana, kumalo kumene munati, Dzina langa ndi kukhalapo kwanga kudzakhala komweko, kuti mumvere mapemphero amene mtumiki wanu adzapemphera atayang'ana kumalo ano. \v 30 Choncho mverani pempho la ine mtumiki wanu ndi la anthu anu Aisraeli pamene tikupempherera kumalo ano. Inde, mverani muli komwe muli, m'Mwamba; ndipo pamene mumvera khululukirani.