nya-x-nyanja_1ki_text_reg/22/18.txt

1 line
465 B
Plaintext

\v 18 Pamenepo mfumu ya Israyeli inati kwa Yehosafati, Kodi sindinakuuze kuti sadzanenera za ine zabwino, koma zoipa zokha? \v 19 Pamenepo Mikaya anati: “Choncho imvani mawu a Yehova: Ndinaona Yehova atakhala pampando wake wachifumu, ndipo khamu lonse lakumwamba litaimirira pambali pake kudzanja lake lamanja ndi lamanzere. \v 20 Ndipo Yehova anati, Ndani adzanyenga Ahabu, kuti akwere nakagwe ku Ramoti Gileadi? Mmodzi wa iwo ananena izi ndipo wina ananena izo.