nya-x-nyanja_1ki_text_reg/22/13.txt

1 line
464 B
Plaintext

\v 13 Ndipo mthenga amene anapita kukaitana Mikaya ananena naye, nati, Taona, mau a aneneri anenera zabwino pamodzi ndi mfumu; mau ako akhale ngati amodzi mwa iwo, nunene zabwino. \v 14 Mikaya anayankha kuti: “Pali Yehova wamoyo, zimene Yehova wanena kwa ine ndinena. \v 15 Atafika kwa mfumu, mfumu inati kwa iye, Mikaya, kodi tipite kunkhondo ku Ramoti Giliyadi kapena tileke? Mikaya anayankha, nati, Menyani ndi kupambana; Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.