nya-x-nyanja_1ki_text_reg/22/10.txt

1 line
493 B
Plaintext
Raw Permalink Blame History

This file contains ambiguous Unicode characters

This file contains Unicode characters that might be confused with other characters. If you think that this is intentional, you can safely ignore this warning. Use the Escape button to reveal them.

\v 10 Ndipo Ahabu mfumu ya Israyeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala yense pa mpando wacifumu, atabvala zobvala zao, pa dwale pa cipata ca Samariya; ndipo aneneri onse anali kunenera pamaso pao. \v 11 Zedekiya mwana wa Kenaana anadzipangira nyanga zachitsulo nkunena kuti: “Yehova wanena kuti, Ndi nyangazi mudzakantha Aaramu mpaka kuwatha.’” \v 12 Aneneri onsewo analosera mofananamo kuti: “Kanthani Ramoti Giliyadi ndipo mudzapambana. Yehova waupereka mmanja mwa mfumu.