nya-x-nyanja_1ki_text_reg/11/07.txt

1 line
301 B
Plaintext

\v 7 Pamenepo Solomoni anamangira Kemosi fano lonyansa la Mowabu malo okwezeka paphiri la kum'mawa kwa Yerusalemu, ndiponso anamangira Moleki fano lonyansa la ana a Amoni. \v 8 Anamangiranso akazi ake onse achilendo malo okwezeka, amene ankafukizapo nsembe zautsi ndi kupereka nsembe kwa milungu yawo.