nya-x-nyanja_1ki_text_reg/11/01.txt

1 line
448 B
Plaintext

\c 11 \v 1 Tsopano Mfumu Solomo inakonda akazi ambiri achilendo, kuphatikizapo mwana wamkazi wa Farao, akazi achimowabu, Aamoni, Aedomu, Asidoni, ndi Ahiti. \v 2 Anali a mitundu imene Yehova anauza ana a Isiraeli kuti: “Musapite pakati pawo kukakwatira kapena kukwatiwa, kapena kuti iwowo asalowe pakati panu, chifukwa adzatembenuzira mitima yanu kwa milungu yawo. Mosasamala kanthu za lamulo limeneli, Solomo anakonda akazi ameneŵa mwachikondi.