nya-x-nyanja_1ki_text_reg/08/54.txt

1 line
479 B
Plaintext

\v 54 Ndipo kunali pamene anasiliza Solomoni kupemphela pemphelo ili lonse ndi kupemphera kwa Yehova, anauka pasogolo pa guwa la nsembe la Yehova, atagwada pansi, ndi manja ake atatambasulira kumwamba. \v 55 Iye anayimirira ndi kudalitsa mpingo wonse wa Israeli mofuwula, \v 56 nati, "Alemekezeke Yehova, amene wapatsa anthu ake Aisraeli mpumulo mwa kusunga malonjezo ake bonse. Palibe mawu amodzi omwe sanakwaniritsidwe pa malonjezo onse yabwino ya Yehova na Mose mutumiki wake.