\v 14 Komanso Yehova adzautsa mfumu ya Isiraeli imene idzaphe banja la Yerobiamu pa tsiku limenelo. Lero ndi tsiku limenelo, pompano. \v 15 Pakuti Yehova adzaukira Isiraeli ngati bango likugwedezeka m’madzi, ndipo adzazula Isiraeli m’dziko labwinoli limene anapereka kwa makolo awo. Iye adzawamwaza kutsidya lina la Mtsinje wa Firate, chifukwa iwo anadzipangira mizati ya Asera ndi kuputa mkwiyo wa Yehova. \v 16 Iye adzasiya Isiraeli chifukwa cha machimo a Yerobowamu, machimo amene anachita, ndiponso amene anachimwitsa nawo Isiraeli.”