\v 6 Ahiya atamva kugunda kwa mapazi ake akulowa pakhomo, anati: “Lowa, mkazi wa Yerobiamu. N’chifukwa chiyani ukudziyerekezera kuti ndiwe munthu? \v 7 Ukauze Yerobiamu kuti, ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndinakukweza pakati pa anthu kuti ndikuike kukhala mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli, \v 8 ndipo ndinang’amba ufumuwo kuuchotsa pa banja la Davide ndi kuupereka kwa iwe monga Davide mtumiki wanga, amene anasunga malamulo anga, nanditsata ine ndi mtima wake wonse, kuchita yekha zoyenera pamaso panga.