\v 29 Choncho Ahabu mfumu ya Isiraeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anapita ku Ramoti Giliyadi. \v 30 Mfumu ya Isiraeli inauza Yehosafati kuti: “Ine ndidzisintha ndi kupita kunkhondo, koma iwe vala zovala zako zachifumu. Chotero mfumu ya Isiraeli inadzisintha + n’kupita kunkhondo.