ny_mrk_text_reg/14/06.txt

1 line
532 B
Plaintext

\v 6 Koma Yesu anati, "Musiyeni mzimai uyu. Cifukwa nicani mufuna kumuvuta uyu? Acita cinthu cabwino kwambimbiri kwa ine. \v 7 Nthawi zonse muzankhala nawo wosauka, ndipo nthawi iliyonse yamene mufuna kuwacitila cabwino muzawacitila, koma simuzakhala naine nthawi zonse. \v 8 Mzimai uyu wacita camene wakwanisha kucita: Wazoza thupi yanga kukonzeka kuikiwa m'manda. \v 9 Zoonadi ndilankhula ndi inu, kulikonse kwamene uthenga wabwino ulalikilidwa kudziko lonse lapansi , camene wacita mzimai uyu, cizalankhulidwa, mokumbukila iye."