\v 11 Koma mukuti, ' ngati munthu akuti kuli atate ake kapena amai ake, "Iliyonse thandizo yocokela kwa ine ni Kobani, "kutanthauza kuti, 'yopasidwa kwa Mulungu')- \v 12 Munthu wotelo musamulole kucita ciliconse kwa atate ake kapena amai ake. \v 13 mulikupanga malamulo ya Mulungu kupanda mpamvu ndi miyambo yanu amene mupasana. Ndizinthu zolingana zimene mucita."