\v 40 Yesu adaima pulu achiwauza kuti munthuyo amubwerese kuna iye. Apo zimolayo atafendera, Yesu adamubvunza, \v 41 Ukufuna ndikuchitire chiyani?'' Iye adati, ''Mbuya, ndikufuna nditambire kupenya kwangu.''