\v 24 Malita adati kuna iye, "Ndikudziwa kuti amdzalamuka pomwe mu mmukiro pansiku yakumaliza." \v 25 Yesu adati kuna iye, "Ndine mmukiro na moyo; iye wakukhulupirira ine, napo achisaika, amdzakhala pomwe na moyo; \v 26 apo aliyense wakukhala na moyo achikhulupirira mwa ine amdzasaika lini. Kodi ukukhulupirira ichi?"